10/10/2026
Good Evening MDzos,
Khalani anthu ofuna kusunga maubale abwino.
Tsiku lina, anthu ena adzanena kuti, “Mwana uyu watengera khalidwe la bambo ake kapena mayi ake.”
Funso ndi lakuti: Mwana wanu adzatha kumwetulira n’kuwayang’ana anthuwo molimba mtima, kapena adzaweramitsa mutu chifukwa cha manyazi ndi chisoni?
Pamene mukukula, muziika patsogolo maubale abwino ndi okhalitsa, osati kuthamangitsa ndalama zokha.
Ndalama zimabwera n’kupita, koma khalidwe lanu, mbiri yanu komanso mmene mumachitira ndi anthu zimasiya chizindikiro kwa ana anu ndi mibadwo ikubwerayi.
Pangani ndalama, koma musawononge maubale. Chuma chenicheni si ndalama zokha, komanso mtendere umene mumakhala nawo ndi anthu.